Anthu ambiri amaona ngati kutchuka kuli ndi ubwino okhaokha ndipo munthu ukatchuka moyo umayenda bwino sumakumana ndi zovuta – koma ayi izi sizili choncho.
Takhala tikumva anthu otchuka ambiri aku Malawi konkuno komanso mayiko akunja akudandaula ndi zinthu zomwe zimawachitikira Kamba ka kutchuka. Inde, mwina kutenga matenda kumene.
Cha pompano, Saint watulutsa nyimbo yake yomwe akuitcha “Fame” momwe walakatula zokhoma zina zomwe munthu ukatchuka umakumana nazo. Koma mwina sioyimba aliyense amane angalakatule zokhoma zomwe amakumana nazo kudzera munyimbo.
Oyimba wa chamba cha hip-hop, Martse sanafune kuchita kulowera ku studio ndikukalakatula zina zoipa zomwe amakumana nazo ngati munthu otchuka.
Iye anapita pa tsamba la mchezo la intaneti la Twitter pomwe anakadandaula kuti monga iye ngati munthu otchuka, zikumamuvuta kupanga zinthu zina mwa chinsisi ngati kuzithandiza chifukwa samapatsidwa mpata okhala pa yekha.
“Being known in Malawi is a struggle…Everyone wants to chill but sometimes I need space koma anthu amangofuna tizicheeeza mpaka kunditsatira ku toilet, “ Martse anafotokoza madando ake.
Masiku amenewa, Martse wakhala akutula pansi nkhawa zake zambiri – inde kudzera pa intaneti komaso mu nyimbo.
Sipakale kwambiri, iyeyu anatulutsa nyimbo yommwe akuitcha “Ndakutulukani” momwe mukumveka kuti anakambamo zinthu zina zomwe zidamupingapinga kanthawi kenakake. Nyimboyi mungaipeze apa