Frank Chawinga anabadwa m’chaka cha 1992, 18 September ku chipatala cha Likuni ndipo wakulira mu m’zinda wa Lilongwe ku Mchesi. Mkuluyi anayamba kuimba ali standard 2 ku Mchesi primary ndipo iye amasilira atamayimba ngati Mlaka Maliro.

Tsiku larelo ife kuno ku Malawi Music tafuna kusakatula ndi kuzukuta mbiri yaka tswiri-tswiri ameneyu Che Wikise.

M’chaka cha 2005 anazakumana ndi m’zake Nitrix m’kupanga gulu loimba, nyimbo yawo yoyamba kuimba inali yotchedwa ndiwe wanga. kenako guluri linasokonekera kamba kazovuta zina. Ndipo Che Wikise anapitiriza kuimba RnB pomwe Nitrix anapitiriza kuimba Hip-hop payekha.

M’chaka cha 2012, anaimba nyimbo kwa Dj Ken Lo yotchedwa “Ukhululuke” kanema wa nyimboyi amaonetsedwa pa Kanema ya MBCtv m’chaka cha 2012 komabe antha sadamudziwe bwino lomwe Wikise.

Mu 2014 mkuluyi anatulutsaso nyimbo yotchedwa “khama” komabe sanatchuke momwe iye am’kafunira. Anthu ochepa okha amkamudziwa Wikise ngakhale kanema wa nyimboyi anaonetsedwa m’makanema ambiri m’dziko muno iye sadatchuke.

Pataita nthawi mkuluyi asanatchuke anagwa ulesi mkuyamba kuchita zinthu zina za moyo wake. Koma mkuluyi sadafooke ndipo anaganiza zoyimba nyimbo ina, nyimboyi ndi yotchedwa Deliverance. Deliverance inatuluka muchaka cha 2017, koma nyimboyi sidafikile anthu ambiri ngakhaleso inaonetsedwa m’makanema am’ziko muno.

Che Wikise before Fame

Patapita miyezi ingapo man Wikise anadya mutu mozama, adaitchakulaso nyimbo ya Deliverance ija mkuiyimba muchamba Trap, ndipo nyimboyi adaisintha dzina mkuitcha Shabarakatakali

Shabarakatali ndi nyimbo yomwe anthu anailandila bwino ndipo mkuluyu anatchuka kwambiri mdziko muno. M’godi ndi wake.

Che Wikise Baba“, anthu ena okonda kunvela nyimbo zake amamutcha Abusa kamba kazisudzo ndi mavalidwe ake amaonetsa munyimbo zake.

Che Wikise anthu ambiri adamudziwa ndi nyimbo yomwe adatchuka nayo muchaka cha 2017 yotchedwa Shabarakatakali. Nyimboyi idamveka kwambiri m’makwalala ngakhale nyimboyi sainaseweredwe kwambiri m’mawailesi am’dziko muno. Kanema wanyimboyi ndiwachikoka chifukwa chazisudzo zomwe zinaonetsedwa ndi Wikese ndi Nzake Akomkala.

Che Wikise Abusa asanapote tsitsi

Che Wikise atango tchuka ndi m’makwalala momwe iye wakhala akutulutsa nyimbo za chikoka ndipo mawu omwe amanveka munyimo zake ama kakhala akugwiritsidwa ntchito polankhula ndi anthu ambiri, mwachitsamzo ” iwe ukufunika Shabarakataliiii, Galamukani man, Osamango lubwa lubwa komaso Uli mzingaaa?”

Che Wikise Watulutsa nyimbo zothentha zingapo monga, Tchimo, Galamukani, Osamangolubwa Lubwa  Likhakhakha komaso Uli Mzingati

“Pakadali Pano Nyimbo yomwe yavuta pa Malawi pano ndi ya Luli Mzingati,, Man Moyo una vuta Man, Uli Mzingati kuti tipange interview yi” Che wikise anatero moselewura Malawi Music team.

 

Subscribe to our Channel on Youtube:

By Malawi Music Team

Winto - Winto Whitelabel. Join Winto - Join Winto. Winto Casino - Review Online Casino Gaming and Demo Gamings. Winto Alliate Network - Best Whitelabel Casino Affiliates. Winto Lottery - iGaming Solutions News

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

giai ma keo nha cai xoc dia tai thien duong tro choi kinh nghiem kiem tien tu ca cuoc the thao phan thuong no hu than tai cach doi tien no hu game 18 teaching feeling keo tai xiu penalty vay ga an thien dom88 tai xiu 93075 bai lieng 3 cay ty le keo bong da tay ban nha responsible gambling rick88 no hu 36804 52 la bai com nemo vin luat choi bai chan tam ly danh tai xiu kham pha thien duong game go88 dang cap va uy tin keo handicap soi keo chelsea