Pa 1 August, oyimba wachinyamata otchedwa Wikise walengeza kuti akutulutsa nyimbo ina yatsopano yomwe akuitcha “Chikamphulikire”.
 
Malingana ndi Katswiriyu, Chikamphulikire ndi nyimbo yomwe ikudzudzula mabwana onse amene amachulutsa kukhomelera (kapena kuti kuika ma inches) kwa anthu omwe anawalemba ntchito mu ma kampani awo.
 
Izi zadza patangotha miyezi iwiri yokha pamene katswiriyu anatulutsaso nyimbo yake ina yotchedwa “Ng’weng’weng’we”.
 
Mu nyimbo ya “Ng’weng’weng’we”, Wikise analakatula nkhalidwe onse omwe azimayi ena olongolora amawachitira azimuna awo.
 
Monga momwe tonse tikumudziwira Wikise, mu nyimbo ya “Ng’weng’weng’we” anawonjezeramoso mseketso wake wa nthawi zonse uja makamaka mu kanema yake yomwe muli Mazzo Openga komanso Seven O More.
Sangalalani ndi kuonera kanemayu pamsipa

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *