Patience Namadingo wadabwa ndi azibambo ena omwe aipidwa mtima ndi nyimbo yake yatsopano yotchedwa “Ng’wii Ng’wii”.

Chitulutsireni nyimboyi pa malawi music website lachiwiri lapitali, pakhala pakumveka kuti kagulu kena ka azibambo sikakukondwa ndi nkhani yomwe waimba katswiriyu munyimboyi.

Koma vuto ndiloti anthuwa sakubwera poyera kuti alongosole kuti madando awo ali pati kwenikweni – chinthu chomwe chadabwitsa Patience Namadingo mpaka pofika kufunsa.

“Koma mwati ma boys Sandimenya zikupitaku? Anyamata ena alusa nayo nyimboyi, pamene pakuwawa kwambili munyimbomu ndipatipati? Girls mwina inu mukupadziwa?” anafunsa chotero Namadingo pa tsamba la mchezo la intaneti lotchedwa Facebook.

Mutha kumvera nyimboyi potsata link iyi – http://m.malawi-music.com/song.php?id=12670

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *