From Left: Hilco & Black Nina

Nkhani yachikondi ndi yovuta kuimvetsetsa ndipo ngati suzitenga bwino zimakathera mu nyimbo.

Atadikira kwa zaka mpaka zinayi kuti mwina Black Nina athira mfundo koma izi osachitika, Hilco anaganiza zolimba mtima ndikupeza mamuna wina pakuti umbeta unali utafika pomukwana.

Black Nina

Mamuna yemwe amadikilira – Black Nina – anali owuma pakamwa kuti akambe zakukhosi.

Izi zadziwika mu nyimbo yatsopano yomwe awiliwa, ayimbilira limodzi yotchedwa “Chidodo”.

Mu nyimboyi, Black Nina wavomereza kufoila kwake kuti adapanga chidodo polephera kufunsira mu nthawi yoyenera.

“Koma ndisaname nthumazi imandigwira ndikamakumbukira zakale ndimangolira/ Lero ndayaluka osakufunsira mpaka zaka 4 kudutsa mwayi uli ngati madzi/ Wai ne unabuduka, kuchulutsa matama kukonda chibwana pano ndinataya nthawi, “Watero Nina pomuuza Hilco.

Hilco

Pomuyankha Nina, mwa mtima wachisoni Hilco wati awiliwa sangakhalireso limodzi pakuti mamuna wina adamutola kale.

“Ukanangolemba kalata mwina ndikanakulora/ Ukanangotuma alonda mwina ndikanawamvera/ Koma Chidodo pano anditenga Ena,” Atero Hilco pa Kolasi ya nyimboyi.

Nyimboyi mutha kuimvera APA

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *